M'chaka cha 2018, bungwe la Results Based Initiative( RBF), lomwe limalandira thandizo la ndalama kuchokera ku mayiko a Germany ndi Norway, lidamanga chipinda cha amayi oyembekezera chatsopano pa chipatala cha pa Mkanda m'boma la Mchinji.
Koma mpaka pano chipindachi sichikugwira ntchito kamba koti katundu yemwe amayenera kubwera pa chipatalachi akuti anapita ku chipatala china, m'boma lomwelo.