UTHENGA OCHOKERA KU MEC
Uthenga wochokera kwa wa pampando wa bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission, Justice Dr. Chifundo Kachale
Moni a Malawi anzanga.
Ndikuthokoza Mulungu chifukwa chotipatsa nthawi yabwino ino kuti tikambirane nkhani zokhudza kuponya voti pa zisankho zapadera zomwe zichitike lachiwiri pa 10 November, 2020 ku madera awa:
• Karonga Central Constituency
• Lilongwe North West Constituency
• Makhwira South Ward ya ku Chikwawa East Constituency
Pachifukwa chimenechi ndikufuna kupereka uthenga wapedera ku dziko lonse, makamaka anthu amene ali m’madera omwe muchitike chisankho chapaderachi. Ndondomeko yonse ili motere:
Ndondomeko yoponyera voti
Malo oponyera voti adzatsegulidwa nthawi ya 6 koloko m’mawa ndikutsekedwa 6 koloko madzulo. Ngati pofika nthawi yotseka padzakhalebe anthu pa mzere, amenewo adzaloledwa kuponya voti, sadzabwezedwa.
Bungwe loyendetsa zisankho likukumbutsa anthu onse kuti, popita kukavota ndikoletsedwa kuvala, kunyamula kapena kupachika makaka aliwonse a chipani kapena a opikisana nawo pa chisankho. Mkulu oyang’anira malo oponyera voti wapatsidwa mphamvu mwa lamulo yochotsetsa wina aliyense opezeka atavala makaka a chipani ngati munthuyo sakuchotsa yekha. Amene adzapite kovota atavala za chipani adzabwezedwa kuti akasinthe ndi kubweranso bwino.
Mukafika kumalo oponyera voti mudzakhala pa mzere. Malo onse oponyera voti komwe kuli anthu oposera 1,000 m’kaundula adzakhala ndi mizere yoposera umodzi. Chonde kaonetsetseni kuti mwayima pa mzere oyenera. Ngati muli ndichikaiko, funsani oyendetsa chisankho kuti akulozereni mzere woti muyime. Nthawi yanu ikafika kuti mukaponye voti, ngati njira imodzi yopewera mlili wa Covid-19, zasambeni m’manja ndi sopo pamalo osambira m’manja omwe bungwe loyendetsa zisankho layika pafupi ndi tebulo loyamba.
Mukafika pa kalaliki woyamba adzakupemphani kuti muonetse chiphaso chanu chovotera. Pofuna kupewa ndi kuchepetsa kufalikira kwa matenda a korona, chiphaso chanucho muzangomuonetsa kalalikiyu ndipo iyeyu adzawerenge chili m’manja mwanu. Kenako kalaliki adzayang’ana dzina lanu mkaundula wavoti. Dzina lanu likadzapezeka mkaundula wavoti, kalalikiyo adzayitana dzina lanu mokweza kuti anthu onse pamodzi ndi oyimira zipani adziwe amene akukavota.
Pamenepo mudzapita pa kalaliki wachiwiri pamene mukabviike chala chanu chankomba phala chakumanja mu inki ndi kupukuta bwinobwino. Inki imeneyi siyowopsya ku moyo wa munthu ndipo ndi chizindikiro chakuti munthu waponya voti.
Mukatero mudzapita pa kalaliki wachitatu pamene akakupatseni pepala lovotera (ballot paper). Ogwira ntchito ya chisankho adzakufotokozerani ndondomeko ya kavotedwe komanso kukuuzani mayina a anthu amene akupikisana nawo pa chisankho. Kuchoka apa mudzapita mu kachipinda komata m’mene mukakhalemo nokha kuti mukasankhe opikisana nawo wa ku mtima kwanu.
Kusankha opikisana nawo pa chisankho
Kuponya voti ndi kwa chinsinsi kotero musaope kapena kuopsyezedwa kuti mudzasankhe munthu amene simukumufuna. Posankha munthu mudzakhala nokha mu kanyumba komata ndipo palibe amene adzadziwe amene mwamusankha.
Kuti musankhe opikisana nawo muyenera kuchonga mu kabokosi kali kumanja kwa chizindikiro cha munthu amene mukumufuna. Onetsetsani kuti chochonga chanu chisatulukire kunja kwa bokosi limeneli. Ngati simungachonge muyenera kudinda ndi chala mkati mwa bokosi limeneli. Onetsetsani kuti musalipake inki pepala limeneli malo ena kupatulapo pamene mwadindapo. Ngati mwangozi inki yapakika malo ena osati amene mumafuna, dziwitsani ogwira ntchito pamalowo kuti akupatseni chipepala china chovotera ndipo choonongekacho muzabweza.
Mukasankha munthu amene mukumufuna, pindani pakati pepala la voti kuonetsetsa kuti mbali yovotera ili mkati. Pindaninso kachiwiri kenako ndi kukayiponya mu bokosi loponyera voti. Mukatero mwamaliza ndondomeko yonse yovota, sambaninso mmanja ndi sopo ndipo nyamukani mudzipita kunyumba kuti mukadikire zotsatira. Simukuloledwa kucheza kapena kumangozungulira pamalo oponyera voti.
Dziwaninso kuti ndikulakwira malamulo kuwulula munthu amene mukufuna kumuvotera kapena mwamuvotera chifukwa voti yanu ndi yachinsinsi. Simukuyeneranso kuonetsa kapena kupanga zizindikiro zoonetsa chipani chimene mumachikonda kapena opikisana nawo pa chisankho amene mumamukonda.
Komanso ndikulakwira lamulo kuwumiriza kapena kunyengerera munthu kuti awulule munthu amene wamuvotera. Aliyense akupemphedwa kuti adziwe za lamulo limeneli.
Kaponyedwe ka voti kwa olumala
Anthu onse olumala adzathandizidwa mwachangu ndipo sakuyenera kuyima nawo pa mzere. Anthuwa akafika pamalo oponyera voti akuyenera akadzionetse kwa oyendetsa chisankho amene adzawathandize kukawakhazika patsogolo.
Chimodzimodzinso kwa amayi oyembekezera, anthu okalamba ndi odwala onse adzathandizidwa msanga. Kwa anthu olumala amene amayenda panjinga asade nkhawa popeza adzathandizidwa kuti aponye voti popanda kutsika pa njinga zawo. Chisankho chikachitikira pabwalo choncho akatha kufikira ndondomeko yonse ya chisankho popanda kufunika kutsika pa njinga.
Kwa olumala m’njira zosiyanasiyana monga kumva kapena kupenya: lamulo likuti anthu oterewo adzabwere ndi munthu amene akumukhulupirira komanso akhale wakuti analembetsa nkaundula wa voti. Munthu ameneyu ndi amene adzawathandize kuponya voti. Ngati sabwera ndi munthu owathandiza, lamulo limanena kuti: mkulu woyang’anira chisankho pa malopo atha kumuthandiza munthu oteroyo.
Pamenepa ndikupempha ma “monitala” onse kuti adzathe kumvetsetsa ndi kutsatira zimene lamulo limanena. Nthawi zina pamakhala kusamvetsetsa kukabwera munthu otereyo chifukwa ma monitala amafuna kuti akaone nawo kuti akumusankhira molondola kapena ayi. Izi zimafafaniza chinsinsi chavoti ndipo ndizoletsedwa m’malamulo.
Pambali pa zimene malamulo akunena, bungwe loyendetsa zisankho lapanga chikombole chomwe chidzathandize kuti anthu amene ali ndi vuto lopenya avote osathandizidwa ndi munthu wina. Pogwiritsa nchito chikombole chimenechi anthu osaona adzatha kusankha wopikisana nawo pa chisankho wakumtima kwawo pogwiritsa ntchito zala zawo. Anthu awa akadzafika polandira mapepala ovotera, kalaliki adzawapatsanso chikombole chimenechi ndi kuwafotokozera m’mene angakagwiritsire ntchito kuti avote. Akatero adzatsogoleredwa kukanyumba komata komwe adzakasankhe munthu wa kumtima kwawo mwa iwo wokha.
Ngati chiphaso cha voti chatayika kapena kuonengeka
Aliyense okavota akupemphedwa kuti adzakumbukire kunyamula chiphaso chovotera. Kwa amene adataya ziphaso zawo, kaya kubedwa, kaya kuonongeka, kapena kulandidwa, ali ololedwa kuponya voti ku malo amene adalembetsera mayina awo mkaundula wa voti.
Akakafika pamalo ovotera ayenera kukadziwitsa oyendetsa chisankho kuti anataya chiphaso chawo. Pamenepo dzina lawo lidzafufuzidwa mkaundula wavoti. Ngati lapezeka adzaloledwa kuvota. Ngati dzina lawo lasowa, sadzaloledwa kuponya voti chifukwa umboni owonetsa kuti analembetsa palibe.
Chitetezo pa malo oponyera voti
Bungwe la MEC lakhazikitsa chitetezo chokwanira. Kumalo onse oponyera voti kudzakhala a Polisi omwe ntchito yawo ndi kusungitsa bata ndi mtendere, pamene chisankho chikuchitika.
Ndichenjeze wina aliyense amene angakhale ndi maganizo ofuna kusokoneza zisankho pamene zili mkati; A Polisi adzakhala tcheru ndipo adzathana ndi wina aliyense oyambitsa ziwawa.
Pempho kwa atsogoleri
Mafumu ndi atsogoleri onse muli ndi udindo waukulu olimbikitsa anthu anu kuti adzapite kukaponya voti kuti adzasakhe munthu owayimirira.
Mafumu ndi atsogoleri amipingo musakondere chipani kapena wina aliyense amene akupikisana nawo pa chisankho.
Kwamakolo ndi aphunzitsi alimbikitseni ana anu omwe analembetsa kuti adzaponye voti yawo, pakuti ichi ndicho cholinga cholembetsera mkaundula wa voti.
Kwa olemba ntchito, ndikupempha mudzawalore anthu anu onse amene adalembetsa mkaundula kuti apite akaponye voti yawo monga njira imodzi yokwaniritsira ufulu wawo.
Pempho la bata ndi mtendere
Ndikulimbikitseni aMalawi amzanga kuti tisunge bata ndi mtendere pomwe mavoti adzakhale akuwerengedwa komanso zotsatira kuwulutsidwa. Ngati munthu adzakhale ndi dandaulo lirilonse lokhudzana ndi chisankho kaliperekeni kwa mkulu oyendetsa chisankho pa malo a voti omwe muli nao pafupi kapena kwa Bwana
Mkubwa wa boma lanu. Iwowa adzakuthandizani moyenera ndithu.
Kuwerenga mavoti
Kuwerengera mavoti kudzayambika nthawi imene kuponya mavoti kwatha. Palibe bokosi limene lidzachoke pa malopo lisanawerengedwe. Oyendetsa chisankho pa malowo ndi anthu okhawo amene adzaloledwe kuwerengera mavoti, ma monitala adzakhalepo panthawiyi kuti adzaonenerere kuwerenga kwa mavotiko.
Dziwani kuti mzere uli onse udzawerengera mavoti paokha ndipo pomaliza mkulu woyendetsa chisankho pa mzere umenewo adzanyamula zotsatira ndi kukapereka ku ofesi ya kwa Bwana Mkubwa wa boma limenelo.
“Monitala” aliyense ayenera kutsimikizira zosatira zonse za pa malopo posayinira ndipo ayenera kukhala ndi zotsatira zofanana ndizomwe zidzatumizidwe ku malo owonkhetsera mavoti. Zotsatirazi adzadzikhoma pamalo pamene voti inachitikira kuti anthu onse adzathe kuona momwe voti yayendera pa malo pamenepo.
Ndipemphe azipani ndi omwe akuyima nawo pazisankhozi kuti awayang’anire mamonitala bwino lomwe kuti adzadzipereke powagwirira ntchitoyi. Ma “monitalawa” alimbikitsidwe kuti asadzachoke pa malo oponya mavotiwa mpaka zotsatira zonse zitawerengedwa ndikusayinidwa. M’mbuyomu taonapo ma “monitala” akuchoka pamalo oponya mavoti pachifukwa choti munthu wawo sakuchita bwino pa chisankhocho. Titsindike kuti siudindo wa “monitala” kupambanitsa opikisana nawo, koma ntchito yake ndi kuonetsetsa kuti zonse zikuyenda mwa dongosolo.
Bungwe loyendetsa chisankho likuyembekeza kuti lidzaulutsa zotsatira lachitatu pa11 November, 2020 zonse zikayenda bwino.
Kupewa matenda a Covid 19
Bungwe loyendetsa zisankho likukumbutsa anthu onse kuti mlili wa
Covid 19 udakalipobe. Chonde pamene mukupita kukavota lachiwiri lino pa 10 November onetsetsani kuti mukutsatira ndondomeko zonse zodzitetezera kutenga ka chirombo ka korona. Njira zake nazi;
• Popita koponya voti onetsetsani kuti mwavala mask kapena chotchinga pakamwa ndi pamphuno. Ngati kuli kotheka zatengeni mankhwala opaka mmanja, kapena kuti hand sanitizer. Komanso ngati nkutheka tengani cholembela chanu.
• Mukafika pa malo oponyera voti onetsetsani kuti mwayima motalikirana mikono iwiri ndi ena. Musapereke moni wa pa manja pamene mwakumana ndi achibale kapena anzanu.
• Pa malo a voti pakakhala madzi osamba m’manja komanso sopo. Mukasamba m’manja onetsetsani kuti mwaumitsa bwinobwino.
• Chiphaso chanu musadzapereke kwa woyendetsa chisankho koma mudzamuonetse ndipo adzawerenge dzina lanu ndi kuona nkhope yanu mutachigwira nokha chiphasocho.
• Onetsetsani kuti pali mpata okwanira pakati pa inu ndi ogwira ntchito ya chisankho komanso oyang’anira chisankho.
• Mukaponya voti yanu kumbukirani kusamba m’manja.
Mulungu akudalitseni pomwe mukukaponya voti yanu la chiwiri lino pa 10 November, 2020.